Isaiah 12

Nyimbo za Mayamiko

1Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:

“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;
chifukwa ngakhale munandipsera mtima,
mkwiyo wanu wachoka,
ndipo mwanditonthoza.
2Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
3Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
4Tsiku limenelo mudzati:

“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
5Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
6Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Copyright information for NyaCCL